5 Uziika magango makumi asanu pa nsaru yocingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; ndipo magango akomanizane lina ndi linzace.
6 Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolidi, ndi kumanga nsaruzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti kacisi akhale mmodzi.
7 Ndipo uziomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; uziomba nsaru khumi ndi imodzi.
8 Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsarukhumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.
9 Nuzisoka pamodzi nsaru zisanu pa zokha ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsaru yacisanu ndi cimodziyo pa khomo la hema.
10 Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru imodzi, ya kuthungo ya cilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru ya kuthungo ya cilumikizano cina.
11 Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.