1 Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wasitimu, utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, guwa la nsembelo likhale lampwamphwa, ndi msinkhu wace mikono itatu.
2 Ndipo uzipanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zikhale zoturuka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa:
3 Ndipo uzipanga zotayira zace zakulandira mapulusa ace, ndi zoolera zace, ndi mbale zowazira zace, ndi mitungo yace, ndi zoparira moto zace; zipangizo zace zonse uzipanga zamkuwa.
4 Ndipo ulipangire made, malukidwe ace ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngondya zace zinai mphete zinai zamkuwa.
5 Nuwaike pansi pa matso a guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.
6 Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi mkuwa.