16 Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zace zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.
17 Nsici zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.
18 Utali wace wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwace makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wace wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsicizo akhale amkuwa.
19 Zipangizo zonse za kacisi, m'macitidwe ace onse, ndi ziciri zace zonse, ndi ziciri zonse za bwalo lace, zikhale zamkuwa.
20 Ndipo uuze ana a Israyeli akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.
21 Aroni ndi ana ace aikonze m'cihema cokomanako, kunja kwa nsaru yocinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israyeli.