20 ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golidi m'zoikamo zao.
21 Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israyeli, khumindiawiri, monga maina ao; monga malocedwe a cosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.
22 Upangenso maunyolo pa capacifuwa ngati zingwe, nchito yopota, ya golidi woona.
23 Nupangire pa capacifuwa mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzika mphete ziwirizo pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa.
24 Numange maunyolo awiri opota agolidi ku mphete ziwiri pansonga pace pa capacifuwa.
25 Koma nsonga zace ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwace.
26 Ndipo upange mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace, m katimo ku mbali ya kuefodi.