28 Ndipo amange capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi,
29 Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israyeli pa capacifuwa ca ciweruzo pamtima pace, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale cikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza.
30 Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza.
31 Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.
32 Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike.
33 Ndipo pa mbinyiru wace upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiirira, pambinyiru pace pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira;
34 mliu wagolidi ndi khangaza, mliu wagolidi ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.