5 Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
6 Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.
7 Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zace ziwiri, kuti amangike nazo.
8 Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
9 Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulocepo maina a ana a Israyeli;
10 maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzace, mwa kubadwa kwao.
11 Uloce miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa nchito ya woloca miyala, monga malembedwe a cosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi,