34 Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza ncopatulika ici.
35 Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ace amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.
36 Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yaucimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakucita coteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.
37 Ucitire guwa la nsembe coteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo a guwa la nsembelo likhale lopatulikitsa; ciri conse cikhudza guwa la nsembelo cikhale copatulika.
38 Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.
39 Mwana wa nkhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo;
40 ndi pa mwana wa nkhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.