1 Koma pamene anaona kuti Mose anacedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.
2 Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolidi ziri; m'makutu a akazi anu, a ana anu amuna ndi akazi, ndi kubwera nazo kwa ine.
3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolidi zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni.
4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nacikonza ndi cozokotera, naciyenga mwana wa ng'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto.
5 Pakuciona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pace; ndipo Aroni anapfuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.