2 Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolidi ziri; m'makutu a akazi anu, a ana anu amuna ndi akazi, ndi kubwera nazo kwa ine.
3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolidi zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni.
4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nacikonza ndi cozokotera, naciyenga mwana wa ng'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto.
5 Pakuciona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pace; ndipo Aroni anapfuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.
6 Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.
7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kucokera m'dziko la Aigupto wadziipsa;
8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwana wa ng'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto,