6 Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.
7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kucokera m'dziko la Aigupto wadziipsa;
8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwana wa ng'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto,
9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;
10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukuru.
11 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawaturutsa m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lolimba?
12 Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.