1 Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekera iwe.
2 Ndipo Yehova ananena naye, Ico nciani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.
3 Ndipo ananena iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa.
4 Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumcira; ndipo anatambasula dzanja lace, naigwira, nikhalanso ndodo m'dzanja lace;
5 kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.
6 Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lace pacifuwa pace, naliturutsa, taonani, dzanja lace linali lakhate, lotuwa ngati cipale cofewa.
7 Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lace pacifuwa pace; naliturutsa pacifuwa pace, taonani, linasandukanso lomwe lakale.