1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2 Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse kacisi wa cihema cokomanako.
3 Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nucinge likasalo ndi nsaru yocingayo.
4 Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zace; ulongenso coikapo nyalico, ndi kuyatsa nyali zace.
5 Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lazolidi cakuno ca likasa la mboni, numange pakacisi nsaru yotsekera pakhomo.
6 Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la kacisi wa cihema cokomanako.