20 Ndipo anatenga mboniyo, naiika mlikasa, napisa mphiko palikasa, naika cotetezerapo pamwamba pa likasa;
21 nalowa nalo likasa m'kacisi, napacika nsaru yocinga, nacinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.
22 Ndipo anaika gomelo m'cihema cokomanako, pa mbali ya kumpoto ya kacisi, kunja kwa nsaru yocinga.
23 Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
24 Ndipo anaika coikapo nyali m'cihema cokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi.
25 Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
26 Ndipo anaika guwa la nsembe lagolidi m'cihema cokomanako cakuno ca nsaru yocinga;