8 Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.
9 Ndipo Mose ananena comweco ndi ana a Israyeli; koma sanamvera Mose cifukwa ca kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.
10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
11 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.
12 Koma Mose ananena pamaso pa Mulungu, ndi kuti, Onani, ana a Israyeli sanandimvera ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?
13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israyeli, ndi za Farao mfumu ya Aigupto, kuti aturutse ana a Israyeli m'dziko la Aigupto.
14 Akuru a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israyeli ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.