15 Ndipo anacotsa milungu yacilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.
16 Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israyeli.
17 Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.
18 Macitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lace kwa Mulungu wace, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli, taonani, zalembedwa m'niacitidwe a mafumu a Israyeli.
19 Pemphero lace lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi chimo lace lonse, ndi kulakwa kwace, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzicepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.
20 Momwemo Manase anagona ndi makolo ace, namuika m'nyumba mwace mwace; ndi Amoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
21 Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri.