2 Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa caka.
3 Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.
4 Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.
5 Mwana wa nkhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa caka cimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.
6 Ndipo mukhale naye cisungire kufikira tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israyeli lizimupha madzulo.
7 Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo.
8 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yooca pamoto, ndi mkate wopanda cotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa,