9 Ndipo Aaigupto anawalondola, ndiwo akavalo ndi magareta onse a Farao, ndi apakavalo ace, ndi nkhondo yace, nawapeza ali kucigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.
10 Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israyeli anatukula maso ao, taonani, Aaigupto alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israyeli anapfuulira kwa Yehova.
11 Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwaticotsera kuti tikafe m'cipululu cifukwa panahbe manda m'Aigupto? Nciani ici mwaticitira kuti mwatiturutsa m'Aigupto?
12 Si awa maowo tinalankhula nanu m'Aigupto ndi kuti, Tliekeni, kuti tigwirire nchito Aaigupto? pakuti kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m'cipululu ai.
13 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, cirimikani, ndipo penyani cipulumutso ca Yehova, cimene adzakucitirani lero; pakuti Aaigupto mwawaona lerowa simudzawaonansokonse.
14 Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala cere.
15 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Upfuuliranji kwa Ine? lankhula ndi ana a Israyeli kuti aziyenda.