8 Ndipondi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,Mayendedwe ace anakhala ciriri ngati mulu;Zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.
9 Mdani anati,Ndiwalondola, ndiwakumika, ndidzagawa zofunkha;Ndidzakhuta nao mtima;Ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.
10 Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;Anamira m'madzi akuru ngati mtobvu.
11 Manana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?Manana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera,Woopsa pomyamika, wakucita zozizwa?
12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja,Nthaka inawameza,
13 Mwa cifundo canu mwatsogolera anthu amene mudawaombola;Mwa mphamvu yanu mudawalondolera njira yakumka pokhala panu poyera.
14 Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira;Kuda mtima kwagwira anthu okhala m'Filistiya.