6 Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israyeli, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakuturutsani m'dziko la Aigupto;
7 ndi m'mawa mwace mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife ciani, kuti mutidandaulira ife?
8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife ciani? simulikudandaulira ife koma Yehova.
9 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.
10 Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli kuti iwo anatembenukira kucipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
12 Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.