13 Ndipo m'kupingasa kwace kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.
14 Ndi nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya kucipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.
15 Ndi pa mbali yina pakhale nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.
16 Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zace zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.
17 Nsici zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.
18 Utali wace wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwace makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wace wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsicizo akhale amkuwa.
19 Zipangizo zonse za kacisi, m'macitidwe ace onse, ndi ziciri zace zonse, ndi ziciri zonse za bwalo lace, zikhale zamkuwa.