26 Ndipo upange mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace, m katimo ku mbali ya kuefodi.
27 Upangenso mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.
28 Ndipo amange capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi,
29 Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israyeli pa capacifuwa ca ciweruzo pamtima pace, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale cikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza.
30 Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza.
31 Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.
32 Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike.