12 Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.
13 Kumbukilani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzichula nokha, amene munanena nao, Ndidzacurukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale colowa cao nthawi zonse.
14 Ndipo Yehova analeka coipa adanenaci, kuwacitira anthu ace.
15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lace; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali yina ndi inzace yomwe.
16 Ndipo magomewo ndiwo nchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.
17 Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kupfuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kucigono.
18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kupfuula kwa olakika, kapena la kupfuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe.