18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kupfuula kwa olakika, kapena la kupfuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe.
19 Ndipo kunali, pamene anayandikiza cigono, anaona mwana wa ng'ombeyo ndi kubvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwace, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
20 Ndipo anatenga mwana wa ng'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli.
21 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakucitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukuru kotere?
22 Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba coipa.
23 Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.
24 Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.