21 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakucitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukuru kotere?
22 Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba coipa.
23 Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.
24 Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.
25 Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,
26 Mose anaima pa cipata ca cigono, nati, Onse akubvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye,
27 Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Yense amange lupanga lace m'cuuno mwace, napite, nabwerere kuyambira cipata kufikira cipata, pakati pa cigono, naphe yense mbale wace, ndi yense bwenzi lace, ndi yense mnansi wace.