3 Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu ali yense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikuru zisadye kuphiri kuno.
4 Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwace magome awiri amiyala.
5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, napfuula dzina la Yehova.
6 Ndipo Yehova anapita pamaso pace, napfuula, Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wacoonadi;
7 wakusungira anthu osawerengeka cifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kucimwa; koma wosamasula woparamula; wakulangira ana ndi zidzukulu cifukwa ca mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai.
8 Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi, nalambira.
9 Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopane pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi ucimo wathu, ndipo mutilandire tikhale colowa canu.