19 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa nsonga ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace m'katimo, pa mbali ya kuefodi.
20 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pace, pa mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.
21 Ndipo anamanga capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.
22 Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, nchito yoomba ya lamadzi lokha;
23 ndi pakati pace polowa mutu, ngati polowa pa maraya ocingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pace, pangang'ambike.
24 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
25 Ndipo anapanga miriu ya golidi woona, napakiza miriu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.