14 Wa Gadi, Eliyasafe mwana wa Deyueli.
15 Wa Nafitali, Ahira mwana wa Enani.
16 Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mapfuko a makolo ao; ndiwo akuru a zikwizo za Israyeli.
17 Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao;
18 nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi waciwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kuchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzi mmodzi.
19 Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'cipululu ca Sinai.
20 Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israyeli, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;