1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndirikupatsa ana a Israyeli; utumize munthu mmodzi wa pfuko liri lonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzace.
3 Ndipo Mose anawatumiza kucokera ku cipululu ca Parana monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akuru a ana a Israyeli.
4 Maina ao ndi awa: wa pfuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri.
5 Wa pfuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori.
6 Wa pfuko la Yuda, Kalebi mwana wa Yefune.