3 Ndipo Moabu anacita mantha akuru ndi anthuwo, popeza anacuruka; nada mtima Moabu cifukwa ca ana a Israyeli.
4 Ndipo Moabu anati kwa akuru a Midyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse ziri pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Moabu masiku amenewo.
5 Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wace, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anaturuka anthu m'dziko la Aigupto; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.
6 Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawalaka, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapitikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.
7 Ndipo akuru a Moabu ndi akuru a Midyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.
8 Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Moabu anagona ndi Balamu.
9 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?