10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
11 Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israyeli, popeza anacita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israyeli m'nsanje yanga.
12 Cifukwa cace nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;
13 ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zace zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anacita nsanje cifukwa ca Mulungu wace, anawacitira ana a Israyeli cowatetezera.
14 Koma dzina la M-israyeli adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba va makolo mwa Asimeoni.
15 Ndi dzina la mkazi Mmidyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkuru wa anthu a nyumba ya makolo m'Midyani.
16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,