14 Koma dzina la M-israyeli adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba va makolo mwa Asimeoni.
15 Ndi dzina la mkazi Mmidyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkuru wa anthu a nyumba ya makolo m'Midyani.
16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17 Sautsa Amidyani ndi kuwakantha;
18 popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'cija ca Peori, ndi ca Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'cija ca Peori.