20 Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israyeli ammvere.
21 Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa ciweruzo ca Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituruka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israyeli pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.
22 Ndipo Mose anacita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse;
23 namuikira manja ace, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose.