6 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
7 Ana akazi a Tselofekadi anena zaona; uwapatse ndithu colowa cikhale cao cao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse colowa ca atate wao.
8 Ndipo unene ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, colowa cace acilandire mwana wace wamkazi.
9 Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ace colowa cace.
10 Ndipo akapanda kukhala nao abale, mupatse abale a atate wace colowa cace.
11 Ndipo akapanda abale a atate wace, mupatse wa cibale cace woyandikizana naye wa pfuko lace colowa cace, likhale lace lace; ndipo likhale kwa ana a Israyeli lemba monga Yehova wamuuza Mose.
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israyeli,