5 ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo, yakutetezera inu;
6 pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, monga mwa lemba lace, zikhale za pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
7 Ndipo tsiku la khumi la mwezi wacisanu ndi ciwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzicepetse; musamagwira nchito;
8 koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya pfungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi; akhale kwa inu opanda cirema;
9 ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;
10 limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;
11 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, pamodzi ndi nsembe yaucimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira.