2 Ndipo maina ao a ana amuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
3 Awa ndi maina a ana amuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao acite nchito ya nsembe.
4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wacilendo pamaso pa Yehova, m'cipululu ca Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anacita Debito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.
5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
6 Sendera nalo kuno pfuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.
7 Ndipo azisunga udikiro wace, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la cihema cokomanako, kucita nchito ya kacisi.
8 Ndipo asunge zipangizo zonse za cihema cokomanako, ndi udikiro wa ana a Israyeli, kuicita nchito ya kacisi.