6 Sendera nalo kuno pfuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.
7 Ndipo azisunga udikiro wace, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la cihema cokomanako, kucita nchito ya kacisi.
8 Ndipo asunge zipangizo zonse za cihema cokomanako, ndi udikiro wa ana a Israyeli, kuicita nchito ya kacisi.
9 Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ocokera kwa ana a Israyeli.
10 Koma uike Aroni ndi ana ace amuna, azisunga nchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
12 Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli m'malo mwa ana ovamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israyeli; ndipo Aleviwo ndi anga.