2 Abwezereni cilango Amidyani cifukwa ca ana a Israyeli; utatero udzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wako.
3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidyani, kuwabwezera Amidyani cilango ca Yehova.
4 Muwatume kunkhondo a pfuko limodzi, cikwi cimodzi, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, atere mafuko onse a Israyeli.
5 Ndipo anapereka mwa zikwi za Israyeli, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.
6 Ndipo Mose anawatuma a pfuko limodzi cikwi cimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Pinehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lace.
7 Ndipo anawathira nkhondo Amidyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.
8 Ndipo anapha mafumu a Amidyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekamu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.