28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akuturuka kunkhondo apereke kwa Yehova; munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.
29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.
30 Ndipo ku gawo la ana a Israyeli utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova.
31 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anacita monga Yehova anamuuza Mose.
32 Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,
33 ndi ng'ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri,
34 ndi aburu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu cimodzi,