5 Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale lao lao; tisaoloke Yordano.
6 Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?
7 Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israyeli kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?
8 Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza acoke ku Kadesi Barinea kukaona dziko.
9 Popeza atakwera kumka ku cigwa ca Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israyeli, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.
10 Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira iye, nati,
11 Anthu adakwerawo kuturuka m'Aigupto, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo; popeza sananditsata Ine ndi mtima wonse;