36 Nacokera ku Ezioni Geberi, nayenda namanga m'cipululu ca Zini (ndiko Kadesi).
37 Nacokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.
38 Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto zaka makumi anai, mwezi wacisanu, tsiku loyamba la mwezi.
39 Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.
40 Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwela m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israyeli.
41 Ndipo anacokera ku phiri la Hori, nayenda namanga m'Tsalimona.
42 Nacokera ku Tsalimona, nayenda namanga m'Punoni.