48 Nacokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikhaza Moabu pa Yordano ku Yeriko,
49 Ndipo anamanga pa Yordano, kuyambira ku Beti Yesimoti kufikira ku Abeli Sitimu m'zidikha za Moabu.
50 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Moabu pa YordaBaku Yeriko, nati,
51 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutaoloka Yordano kulowa m'dziko la Kanani,
52 mupitikitse onse okhala m'dzikopamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;
53 ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanu lanu.
54 Ndipo mulandire dzikoli ndi kucita maere monga mwa mabanja anu; colowa cao cicurukire ocurukawo, colowa cao cicepere ocepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwace; mulandire colowa canu monga mwa mapfuko a makolo anu.