14 popeza pfuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi pfuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi pfuko la hafu la Manase lalandira colowa cao;
15 mapfuko awiriwa ndi hafu adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano ku Yeriko, kum'mawa, koturukira dzuwa.
16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
17 Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale colowa canu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18 Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku pfuko limodzi, agawe dziko likhale colowa cao.
19 Maina a amunawo ndiwo: wa pfuko la Yuda, Kalebi mwana wa Yefune.
20 Wa pfuko la ana a Simeoni, Semuyeli mwana wa Amihudi.