4 ndi malire anu adzapinda kucokera kumwela kumka pokwera Akrabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kuturuka kwace adzacokera kumwela ku Kadesi Barinea, nadzaturuka kumka ku Hazara Adara, ndi kupita kumka ku Azimoni;
5 ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kumka ku mtsinje wa Aigupto, ndi kuturuka kwao adzaturuka kunyanja.
6 Kunena za malire a kumadzulo, nyanja yaikuru ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.
7 Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku nyanja yaikuru mulinge ku phiri la Hori:
8 kucokera ku phiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kuturuka kwace kwa malire kudzakhala ku Zedadi.
9 Ndipo malirewo adzaturuka kumka ku Zifironi, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Hazara Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
10 Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ocokera ku Hazara Enani kumka ku Sefamu;