8 kucokera ku phiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kuturuka kwace kwa malire kudzakhala ku Zedadi.
9 Ndipo malirewo adzaturuka kumka ku Zifironi, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Hazara Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
10 Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ocokera ku Hazara Enani kumka ku Sefamu;
11 ndi malire adzatsika ku Sefamu kumka ku Ribala, kum'mawa kwa Ayina; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
12 ndi malire adzatsika ku Yordano, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Nyanja ya Mcere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ace polizinga.
13 Ndipo Mose anauza ana a Israyeli, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kucita maere, limene Yehova analamulira awapatse mapfuko asanu ndi anai ndi hafu;
14 popeza pfuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi pfuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi pfuko la hafu la Manase lalandira colowa cao;