7 Ndi pa gome la mkate waonekera ayale nsaru yamadzi, naikepo mbale zace, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa cikhalire uzikhalaponso.
8 Ndipo ayale pa izi nsaru yofiira, ndi kuliphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.
9 Ndipo atenge nsaru yamadzi, ndi kuphimba coikapo nyali younikira, ndi nyali zace, ndi mbano zace, ndi zaolera zace, ndi zotengera zace zonse za mafuta zogwira nazo nchito yace.
10 Ndipo acimange ndi cipangizo zace zonse m'cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa conyamulira.
11 Ndipo pa guwa la nsembe lagolidi aziyala nsaru yamadzi, naliphimbe ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.
12 Natenge zipangizo zace zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsaru yamadzi, ndi kuziphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika paconyamulira.
13 Ndipo azicotsa mapulusa pa guwa la nsembe, ndi kuyala pa ilo nsaru yofiirira.