1 Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa kacisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;
2 akalonga a Israyeli, akuru a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mapfuko akuyang'anira owerengedwa;
3 anadza naco copereka cao pamaso pa Yehova, magareta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi ng'ombe khumi ndi ziwfri; akalonga awiri anapereka gareta mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa kacisi.
4 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
5 Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakucitira nchito ya cihema cokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa nchito yace.