2 akalonga a Israyeli, akuru a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mapfuko akuyang'anira owerengedwa;
3 anadza naco copereka cao pamaso pa Yehova, magareta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi ng'ombe khumi ndi ziwfri; akalonga awiri anapereka gareta mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa kacisi.
4 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
5 Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakucitira nchito ya cihema cokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa nchito yace.
6 Ndipo Mose analandira magareta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi.
7 Anapatsa ana a Gerisoni magareta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa nchito yao;
8 napatsa ana a Merari magareta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa nchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.