20 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
21 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
22 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
23 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Netaneli mwana wa Zuwara.
24 Tsiku lacitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni:
25 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
26 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;