34 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
35 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elizuri mwana wa Sedeuri.
36 Tsiku lacisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiyeli, mwana wa Zurisadai:
37 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
38 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
39 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
40 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;