80 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
81 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
82 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
83 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ici ndi copereka ca Ahira mwana wa Enani.
84 Uku ndi kupereka ciperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israyeli, tsiku la kudzoza kwace: mbizi zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolidi khumi ndi ziwiri;
85 mbizi yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
86 Zipande zagolidi ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi cofukiza, cipande conse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golidi wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;